Apha mzake chifukwa cha hule

Advertisement
CUFF

Mnyamata wina wa zaka 18 mu boma la Chikwawa amunjata atapha mzake ati polimbilana mkazi oyendayenda.

Malinga ndi mneneri wa a Polisi mu bomali a Foster Benjamin, ati upanduwu udachitika pachinayi pamene abambo awiri amamwa mowa mmudzi wina mu bomalo.

MachingaA Malora Fulingi amene atsekeledwa ati anapita ku mowa, ndipo ali kumene kuja anadyelera maso pa hule. Iwo akuzembelera, mzawo wina adapezeka kuti wapana hule uja.

Apo ati mkangano unabuka, ndipo a Fulingi pochepa mphamvu anatenga mwala nagenda nawo a Wilfred Billiat a zaka 20 amene anali atapana hule amakanganilanayo.

A Billiat anagwa ndi kukomoka ndipo anatengeledwa kuchipatala komwe anatsamaya pachiweru.

Padakali pano a Fulingi ali mmanja mwa apolisi ndipo akuyembekezeleka kukaonekela ku khoti kumene akayankhe mulandu okupha.