Apha mzake chifukwa cha hule

Advertisement
Machinga

Mnyamata wina wa zaka 18 mu boma la Chikwawa amunjata atapha mzake ati polimbilana mkazi oyendayenda.

Malinga ndi mneneri wa a Polisi mu bomali a Foster Benjamin, ati upanduwu udachitika pachinayi pamene abambo awiri amamwa mowa mmudzi wina mu bomalo.

MachingaA Malora Fulingi amene atsekeledwa ati anapita ku mowa, ndipo ali kumene kuja anadyelera maso pa hule. Iwo akuzembelera, mzawo wina adapezeka kuti wapana hule uja.

Apo ati mkangano unabuka, ndipo a Fulingi pochepa mphamvu anatenga mwala nagenda nawo a Wilfred Billiat a zaka 20 amene anali atapana hule amakanganilanayo.

A Billiat anagwa ndi kukomoka ndipo anatengeledwa kuchipatala komwe anatsamaya pachiweru.

Padakali pano a Fulingi ali mmanja mwa apolisi ndipo akuyembekezeleka kukaonekela ku khoti kumene akayankhe mulandu okupha.

Advertisement

32 Comments

  1. Za ziiiiiiiiii wakuchita chimo akhala kapolo wa tchimo ameneyo ayisovange.Munthu kuti atchedwe Hule ndiye kuti amagonana ndi amuna ambiri ndipo mwa iye muli matenda sizopherana izi za ziiiiiiiiii.

  2. Uku Ndko Kupepera Mzeru Hule Sichinthu Chomenyanirana Mpaka Kupha Mzako Kungokwatira Bwanj Ngat Ukuona Kt Wafikapo Zopusa Ngt Zmenez

    1. Kkkkkkkkkk chamba kwambiri awa ana a ku chikwawa…..zaaaziiiiiiii

  3. kodi moyo umaona ngati ndiongotola padzala eti? moyotu ndiodula nchifukwa chani kumaseweletsa moyo wanzako choncho? nanga kodi uhule ndi nsima kapena mpunga kuti mutha kutigailako nafe, muzisamala pochita zinthu coz Jesu is coming very soon.

  4. Anayambisa ndeu ndiophedwayo koma phamvu zoti angamenyane ndi nzakeyo analibe sikut chinalicholinga ayi koma amamenyana

  5. Kumeneko ndiye timati kupanda nzeru, Kuononga moyo wam’zako chifukwa cha mkazi, wagulu; woti siwakowako?? Tsono wapindulanjipo; poti kumene akulowerako ndi (half grave) kale, or akanadikira turn yake siikanabwera?

Comments are closed.