Wa Kongeresi ndani? Ine ndi oyima payekha – Anong’a apotoloka

Advertisement

Sanachiteko olo msonkhano umodzi oitanila anthu ku chipani. Olo kuvala makaka a chipani sanachiteko.

Osewela mu timu ya Bullets amene tsopano walengeza kuti mtima wake uli pa ndale, Anong’a Fischer Kondowe wanena kuti iye ndi oyima payekha.

Kondowe wanena kuti iye ndi oyima payekha.

Kondowe wanena izi patangotha ma ola chabe a Sidik Mia atamulandila ku chipani cha Kongeresi.

A Mia amalandila anthu amene aonetsa chidwi choimila Kongeresi mu chisankho cha 2019 ndipo mmodzi mwa anthuwa anali a Kondowe amene akufuna kuyimila pa mpando wa uphungu ku dera la Kum’mwera mu boma la Blantyre.

“Ine anangondiyitana ku msonkhano wa atolankhani, sitinakambilane zolowa mu chipani,” anatelo Kondowe polengeza za kupotoloka kwake.

Iye ati tsopano ndi okonzeka kugwila ntchito ndi zipani zonse osati Kongeresi yokha.

Advertisement

53 Comments

 1. Anong’a nzeru zako siudakhwime and waoneselatu kuti azikugwedeza aliyense obwera, chifukwa chisankho siudapange. Dziwa kuti mmera mpoyamba ndipo ukachedwa anzako atola khobwe ukuliyayalo kenako udzalira madzi atachita kale katondo

 2. Ine mdanenapo kale kuti uyu mukuti Jahmanyu sangakalowe mparliament ndi tsitsi lake losapesa kuti adzikachita mbwerera zake zimenezi. Akungofuna kupusitsa anthu uyu kapena afuna achite fundraise… Mmmmmmh.

 3. FISHA PAMENE ANALENGEZA KUTI AYIMILA MCP AMBILI ANAYAMIKILA BUT NOW WASINTHA THASWHY AMBILI AKWIYA KOMATU MUWELENGE MAKOMENT ,PAMENEPO NDIPAMENE MUNGAWONE MAVOTI AFISHA ,MUNTHU SUNGASIYE CHIPANI CHAKO KUKAVOTELA WOYIMAPAYEKHA NANGA POTI ZAWONEKAKALE KUTI NDICHENJIGOLO MAWA AKALOWA KUCHIPANI

 4. Chamba chake chimenechi azikapanga ku Parliament ndiye dziko lingtukuke??….a Malawi tikuyenela kuzindikila kuti ngati tikufuna kuti dzikoli litukuke tikuyenela kukhala osamala pa anthu omwe tikuwasankha kukhala adindo zomasankha munthu kamba kachisoni kapena jst for morale dziko la Malawi lidzakhala laumphawi mpaka kale kale, a Malawi sitimakhala serious pakachitidwe kazinthu that’s why Malawi amangozungulira malo a modzi modzi…Ngati tikufuna dziko lathu litukuke we need change our mindset and mentality we need to be strong in our thinking capacity and in decision making let’s be tired of dancing the same old songs anthu ngati awa tawayesapo ndipo atilephera ndipo ena ndi awa akutizunzawa we need to get a lesson and say enough is enough!

 5. ine mdakakonda mtafunsako anthu akuchilobwe ngati mukundimva pano kd fisher kuyambila kale ndiwachipani chanji? vuto pa fb pano timangopusisanapo mwachitsano nd olemekeze alucius banda akangolemba nkhan yotsutsana nd boma macoment amakwana khumi mkumwendo pano koma akangolemba zoyamikila boma palibe amacomenta pano ndiye fisher ngati ukundimva panga zako usamvele zapafb pano anthu onse akuti chambawa sakhala kuchilobwe ndichamba chakocho panga zot usangalase anthu akwanu bas zitamveka kt walowa mcp dzana anthu ambir amat wanyika lerons akukamba zina malawi amoto ndi amenewo

 6. Ubwino wake wake anthu amabwela okha ku mcp simagula anthu ndiye ngati anali fodya adzava kuwawa 2019 ife tikupita ku kenani mcp 2019ukudziwa kale wekha kuti ndi boma

 7. Fodya si wa bwino, makamaka uyo asutayo eish.
  Ndipo ku parliament kumapita anthu olankhula chizungu nde awa chingerezi chawo . (2) Kumapita anthu a descent, nde ma dreadi yalakwa. George Weah anapita ku sukulutu.

 8. Musiyeni munthu kunali kuyamba kugwilana chanza ndili Munthu wotchuka komanso wandalama zake ndiye mwina amaganiza ngati amupatsa poyambila. Koma ndingomupempha kuti akhazikise mtima pansi & apange chisankho cholondola

 9. Eeee koma chambachi mukazawina ndiye kuti muzasegula mafakitale achamba kumalawi kuno mwina anthu azalemelako kkkkkkkkkkkkk sopano mia udakumana nawo utabandika kwambili ? Kuti sumaziwa chomwe chimachitika

Comments are closed.