A Kongeresi ati akola chambo, a DPP ati ndi chule ameneyo

Advertisement

Eni ake akolawo ali ndi chimwemwe kuti akhwasula, kuti mavoti onse a Kum’mwera kwa mzinda wa Blantyre tsopano akhala awo. Koma kwa aneba awo ndiye kuli phwete.

Pamene ndale zafika pa chi inde inde, chipani cha Kongeresi chalengeza kuti chalandila mu chipanichi Anong’a Fischer Kondowe.

a Mia kulandila Fischer Kondowe mu MCP.

Kondowe amene ndi katswiri wa mpira wakhala akulengeza kuti iye wapanga chisankho choyamba ndale. Iye wati 2019 akhala akupikisana nawo pa mpando wa uphungu ku dera la Kum’mwera mu Blantyre kumene phungu wake pakali pano ndi a Allan Ngumuya.

Pamene Kondowe amalengeza za maloto ake, iye sanatchule chipani chomwe ayimile koma tsopano zadziwika.

Kondowe walandilidwa ku chipani cha Kongeresi ndi Bambo Sidik Mia amene akuoneka kuti atha kuzakhala wachiwili wa Bambo Chakwera mu 2019.

Anthu a Kongeresi akuoneka osangalala pa Facebook ndi kubwela kwa Anong’a. Zikuoneka ngati kwa iwo Anong’a ndi Khang’a amene awabweletsele mavoti.

Pamene a Malawi24 tinalemba nkhaniyi mu chizungu, anthu angapo okonda Kongeresi ananyadila.

“Mwachita bwino Jah man, mwasankha chipani chowina,” analemba choncho a Steve Nzati.

A Fred Matabwa nawo anamuyamikila kuti Kondowe ndi olimba mtima ndipo wapanga chisankho cha nzeru.

Koma anthu ambiri a DPP aseka ndi ganizo la Kondowe.