Amusasantha, amugweba, amutsinatsina neba lero

Advertisement

Kokuba mifuti sitipita ndi utsi wa fodya basi. Poputa asilikali, kumazimitsila nduduzo. Maule atuluka.

Ndi Kamuzu Barracks ndi Moyale amene atsala kulimbanilana ukulu wa chikho cha FISD. Zivute zitani achitenge ndi asilikali basi.

Moyale Barracks
Moyale yasasantha Bullets

Timu ya Bullets lero yaonetsedwa zoopsa itatibulidwa ndi asilikali a ku Kaning’ina mu chikho cha FISD.

Pa masewelo amene anachitikila pa bwalo la za masewelo la Civo mu Mzinda wa Lilongwe, anayamba kuonetsa chamuna anali anyamata a Moyale amene anamwetsa chigoli patadutsa mphindi makumi awiri.

Anali mnyamata Khuda Muyaba amene anadzetsa chidima ku banja la maule, kuwasiyila chizilezile mmaso.

Maule anaphukilamo mu chigawo chachiwiri pamene mnyamata wawo Chiukepo Msowoya anamwetsa chigoli kuti ayike masewelo pa 1 kwa 1.

Zinaoneka ngati maule atchola ku Barracks lero pamene anapeza penote. Fischer Kondowe anamwetsa ndithu ndi kuika maule patsogolo.

Koma chisangalalo cha maule chinafanana ndi cha munthu ochimwa chifukwa chinangokhala kwa ka nthawi kochepa chabe.

Anyamata a Moyale anabwelanso ndi ukali ndi kuthila mpholopolo kwa Ma palestina kupangitsa kuti masewelo afike ku kaphelachoka, ma penote.

Uku ndiko maule aona mbonaona, atsanzikana ndi chikho cha FISD.

Pamene Moyale inaonetsa ukadaulo ogoletsa ma penote, Nelson Kangunje wa Bullets anachita njengunje ndi kuphonya.