‘Ndani akufuna kumwa tudziyo? Ine ayi…’ nduna ikana madzi a ku 18

Advertisement
Dausi

Ngakhale a bungwe loona za madzi mu Lilongwe la Lilongwe Water Board linanena kuti madzi a ku Area 18 atha kumwedwa tsopano, nduna ya zofalitsa nkhani a Nicolas Dausi ati iwo sangamwe madzi otuluka ku deralo.

Sidik Mia
Dausi: Wati sangamwe madzi a ku Area18.

A Dausi ananena izi lamulungu pocheza ndi mtolankhani wina pa wailesi.

Pa nkhani ina imene iwo anafunsidwa monga mneneri wa boma inali yokhudzana ndi madzi a ku Area 18.

Iwo analangiza anthu a ku Area 18 kuti amvele langizo la anthu a ku Water Board amene akunena kuti madzi a kumeneko ndi oyenera kumwedwa tsopano.

Koma atafunsidwa ngati iwo angamwe madziwo, a Dausi anachita njengunje ndi kunena kuti nkhani imeneyo akuyenela kufunsidwa ndi a ku Water Board.

Iwonso anatsindika kuti sangamwe madzi a ku 18.

Advertisement