Kuli demo ya mahule

Advertisement
prostitution malawi

Amayi oyendayenda ati achita zionetselo zosonyeza kukwiya ndi nkhanza zimene amakumana nao akamagwila ntchito yawo usiku.

A Zinenani Majawa amene ndi wamkulu wa bungwe la amayi oyendayenda ndiwo alengeza zoti ma membala a bungwe lawo ndi okonzeka tsopano kutenga zida ndi kuthana ndi mchitidwe wa nkhanza umene amakumana nawo.

sex-workers-new
Amayi oyendayenda aopseza kuchita zionetselo.

Iwo ati apolisi ndi anthu ogwila ntchito mu chipatala ndiwo ali patsogolo ndi mchitidwe wa nkhanza kwa amayi oyendayenda usiku.

‘Amayi ambiri oyenda usikufe tikukumana ndi nkhanza, apolisi ndi azachipatala ali patsogolo pochita nkhanza zimenezi. Posachedwapa mumva tikuchita zionetselo ngati anthu amenewa sasintha,’ atelo a Majawa.

A bungwe loona za ufulu wa anthu la CHR mu boma la Salima ati ndi zoona zoti amayi oyenda usiku akuzunzidwa. Iwo anati amayiwo awadandaulilapo kochuluka ndipo akumvetsa chifukwa chimene amayiwa akufuna kuchita zionetselo.

A Majawa ati mu sabata ziwiri zikudzadzi akhala akukumana ndi akuluakulu apolisi komanso a ku unduna wa za umoyo ndipo awadandaulila mavuto awo ndipo ngati pasowe chochitika, basi iwo akupita pamseu.

 

 

 

 

 

Advertisement