Bullets inauka ija yafanso pamene nyerere zakwilila kwa dzulo

327

Chaka chino si cha maule. Ataoneka kuphukila sabata latha mpaka ena kumati azitolela, maule apezanso mavuto lero mu mzinda wa Lilongwe.

Pa masewero amene anali ovuta a pakati pa Bullets ndi Silver, akatswiri a ku Blantyre abwera chimanjamanja atakwapulidwa ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi.

Malawi football bullets silver strikers fc

Bullets yafa kwa Silver

Kunali kupsetsana mtima ndi chimkulilano matimuwa atakumana koma pakutha pa zonse, a Silver anali ataonetsa kuti akamuna ndi iwo ndipo kugonja kwa pa 6 July kuja kunali chibwana basi.

Masewelo amenewa anaonanso zipolowe pamene mapalestina otopa anagenda miyala kwa Masapota a Silver.

Ku Dedza, manoma akonza kwa dzulo atagonjetsa Masters Security.

Dzulo nyerere zinanyozeka zitagonja kwa Civil ndi zigoli ziwiri kwa duu koma lero yakwilila chitonzo chija.

Share.
  • Opinion