A Mutharika athawa

Advertisement
Peter Mutharika

Abanduka dzulo kulisiya dziko liri pamoto.

Pamene aphunzitsi a ku Primary komanso ena a ku Secondary anyanyala ntchito, mtsogoleri wa dziko Peter Mutharika lino wathawanso kumapita kunja.

A Mutharika anyamuka ku Malawi dzulo masana ati kupita ku Brussels, mu dziko la Belgium.

Peter Mutharika
A Peter Mutharika atuluka dziko muno.

Akuti akachoka kumeneko, a Mutharika apita ku London mu dziko la England kumene akayankhule kwa ophunzila a pa sukulu ya ukachenjede ya Oxford.

Ati ku sukulu ya Oxford a Mutharika akayankhula pa nkhani yokhudza maphunziro. Izi zili chonchi ngakhale iwo boma lawo likukanika kupeleka maphunziro.

Ulendo wa a Mutharika wakwiyitsa a Malawi angapo amene aona kuti iwo angoononga ndalama.

“Nthawi zonse mkulu ameneyi akamachoka, amatinamiza kuti akapindulila dziko koma phindu lake sitiliona mpaka pano,” anatelo a Ntata.

Advertisement