Nyerere zikokela jombo kuuna

Advertisement
Felix Zulu

Zaiboolatu jombo ija, ndi kuichecheta mpaka kuthawila nayo kuuna.

Timu ya mpira wa miyendo ya Be Forward Wanderers dzulo yamwetsa wamkaka oitsatila pamene inachita zodabwitsa mu mzinda wa Lilongwe.

Manoma amakutumulana ndi timu ya Moyale mu ndime ya chipulula ya chikho cha Top 8.

Felix Zulu
Manoma awina ndi Moyale.

Masewelowa anayamba ndi kukomela asilikali a Moyale amene anamwetsa chigoli kudzela mwa mnyamata wawo Boyboy Chima.

Pofuna kutsila Actelic kuuna kuti nyerere zifele komko, anyamata a Moyale anaomba mpholopolo wachiwili kudzela mwa mnyamata Dan Katunga.

Koma akanadziwa asilikaliwo sakanaziputa nyerere. Patatsala mphindi ziwiri kuti chigawo choyamba chithe, Khumbo N’gambi anaika mu ukonde mpira kuti abweletse chimwemwe kwa manoma.

N’gambi anamwetsatso china mu chigawo chachiwiri ndipo pofuna kuonetsa kuti iye saizi ikukana, anakhoma msomali omaliza pa bokosi la asilikali.

Pofika pamapeto, nyerere zinawadutsa asilikaliwo ndi kupambana 3 kwa 2.

Izo zikuyembekeza zotsatila za tsiku la lero za pakati pa Siliva ndi KB kuti adziwe opambana amene azakumane naye mu chigawo chomaliza.

Advertisement

2 Comments

  1. Yasin Osman must be saluted for showing asilikali kuti iye ndi katswiri pa nkhani ya mpira. Moyale munachepa nazo afunseni a neba….kkkkkkkkkkk.Wagwa nayo mfunti..sssssssssssshhhaame..

Comments are closed.