Nkhani ya ma kondomu achikazi ivuta: amayi akuwakana ati amaononga chisangalalo

76

Akatswiri pa nkhani ya uchembele wabwino adandaula  kuti ma kondomu achikazi sakugwilitsidwa ntchito pamene zikuoneka kuti anthu achizimayi akuchita chowazemba.

Izi zaululika pa msonkhano wina omwe unachitika mu boma la Mzimba.

female-condoms

Makondomu amayi akukanidwa.

Poyankhula pa msonkhano umenewu, mkulu othandizila pa nkhani ya ubeeleki wabwino a John Msiska anati makondomu achikazi sakugwiliitsidwa ntchito.

“Angotikhalilatu mu zipatala umu makondomu amenewa, mpaka akuchita fumbi,” anatelo Msiska.

Iye anapempha amayi kuti akuyenela kuyamba kugwilitsa ntchito makondomu amenewa kuti aziteteze ku matenda komanso ngati njira imodzi yolela.

Koma amayiwo atatenga bwalo kunaphulika nkhani. Mayi wina anaima ndi kunena kuti makondomu achikazi si abwino chifukwa amasokoneza ntchito ya ku chipinda.

“Makondomu amenewa si dhilu ayi, munthu ukatchena ntchito yak u chipinda ija osalongosokanso ayi,” anatelo mayi wina.

Anzake anagwilizana naye.

Mayi wina anaonjezela kuti iwo amachita manyazi kukatenga ku chipatala.

Share.
  • Opinion