25 October 2016 Last updated at: 10:08 AM

A Mutharika anangotha nthawi ndi msonkhano wa atolankhani uja – atero otsutsa

Peter Mutharika

Peter Mutharika: Wathiidwa mphepo.

Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika adzudzulidwa mwamphamvu ndi atsogoleri ena otsutsa ati kamba kotayitsa nthawi a Malawi ndi msonkhano wa atolankhani umene anachita lachisanu sabata yatha ku nyumba ya boma mu mzinda wa Lilongwe.

Malingana ndi mtsogoleri otsutsa mu nyumba ya malamulo, a Lazarus Chakwera, a Mutharika anangobweleza zimene anthu akudziwa kale mmalo monena mau a tsopano opeleka chiyembekezo kwa a Malawi.

A Chakwera anapsela mtima a Mutharika ndikuwadzudzula ati kamba kobisa nkhani ya matenda awo amene.

“Iwo asaname, anakhalitsa mu dziko la Amereka chifukwa cha matenda awo osati kuti amagwila ntchito zina zaboma, koma taonani mmene anayichitila nkhani ija. Anangowawula basi,” anadandaula motero a Chakwera.

A Chakwera ananena kuti khalidwe la a Mutharika lobisa matenda ndi limodzi mwa zifukwa zimodzi zimene a Malawi akufunila lamulo lopeza nkhani ku boma lija pa chingelezi akuti ATI bill.

John Chisi

Chisi; Mutharika sanalankhule zomveka.

“Tikanakhala ndi lamulo limeneli ndipo likugwila ntchito yake moyenela, a Malawi sakanavutika chonchi,” anatelo a Chakwera.

Kumbali yawo a John Chisi amene ndi mtsogoleri wa umodzi anadzudzula a Mutharika ati kamba kouza atolankhani kuti ngati akufuna ayimbe munthu mlandu pa kubisa za kumene anali amayenela kuyimba iwo basi.

“Boma si munthu mmodzi iyayi, boma ndi anthu ambiri. Iwo akunena bwanji kuti tiyimbe mlandu iwo wokha. Iwo akuziyetsa ndani kodi?” anatero a Chisi.

A Chisi anati mawu a Mutharika anali oloza ku chipani chimodzi zimene zili zosaloledwa.

A Mutharika adalankhula ndi atolankhani lachisanu patatha masiku asanu iwo atafika mu dziko muno kuchokela ku msonkhano wa UN ku dziko la Amereka.  182 Comments On "A Mutharika anangotha nthawi ndi msonkhano wa atolankhani uja – atero otsutsa"