23 October 2016 Last updated at: 10:38 AM

Sindipepesa – atero a Ndau pokhudzana ndi matenda a Mutharika

Peter Mutharika

Peter Mutharika -Adati adali ndi nyamakazi.

Nduna yoona zofalitsa nkhani imenenso ili mneneri wa boma a Malison Ndau auza atolankhani ndi mabungwe ena amene amafuna kuti iwo apepese ati kamba koti ananena bodza pa za umoyo wa mtsogoleri wa dziko lino kuti iwo sangapepese.

Mabungwe ena omwe si a boma anakhala akuyimba milandu a Ndau kuti apepese pouza mtundu wa a Malawi kuti a Peter Mutharika ali ndi moyo wangwiro ku Amereka. Koma a Mutharika atabwela ananena kuti io nyamakazi inawasautsa ku Amereka kutanthauza kuti amadwala.

Koma poyankhulapo pa nkhaniyi, a Ndau amene amanenela boma ndipo anaopseza kuti anjata anthu amene anali kutchukitsa kuti a Mutharika anali akudwala anayankhula kuti sangapepese.

Malison Ndau

Malison Ndau: Sindingapepese.

“Ine sindinaname iyayi, ine ndimanenela boma ndipo ndinanena zimene a boma amadziwa. Ku boma timadziwa kuti a Mutharika ali wangwiro ndipo sitinaname konse,” anatero a Ndau.

“Choyenela kudziwa ndi choti a Mutharika ali ndi moyo wawo umene pena umayenda opanda a ku boma kudziwa, nkhani ya matenda iyi sitinauzidwe poti sanali matenda enieni,” anaonjezelapo a Ndau.

A mabungwe anapsela mtima a Ndau ati chifukwa ananena kuti Mutharika ndi wangwiro koma mwini wache ananena za nyamakazi. Koma ngakhale zili choncho, a Mutharika ananena kuti nyamakazi imene inawavuta sinali vuto kwenikweni.

“Kanali chabe ka nyamakazi kamene kanavuta, ndipo ine ndikudziwa palibe munthu anafapo ndi nyamakazi kupatula mwina ku Zodiak,” anatelo a Mutharika polankhula ndi atolankhani lachisanu.

A Mutharika anakhala ku dziko la Amereka misonkhano imene anapitila itatha. Iwo anaonjezela kukhala kwawo ndi masabata awiri. Izi zinapangitsa anthu kuyamba kufalitsa nkhani.

Zinatchukitsidwa kuti a Mutharika akudwala. Iwo atabwela mdziko muno anaonjezela mphekesela izi pokanika kugwilitsa ntchito mkono wawo ma dzanja la manja.95 Comments On "Sindipepesa – atero a Ndau pokhudzana ndi matenda a Mutharika"