Lucius Banda Sanagugepo

Advertisement
Soldier Lucius Banda

Bugwe la Copyright Society of Malawi (COSOMA), kudzera mwa wapampando wa bungweli a Chimwemwe Mhango, ati Lucius Banda sanagugepo chiyambileni kuyimba kwake  zaka zoposa 30 zapitazo, zomwe zukuwonetseratu mphamvu zomwe Mulungu anamupatsa pa kapekedwe komanso kayimbidwe kake ka nyimbo ku Malawi.

Mu ma uthenga a kulira kwawo pa  mwambo wa maliro a katswiri wa zimbale 20-yu pa  bwalo la Balaka m’bomali, a Mhango ati mkofunika kuti dziko likhale ndi ndondomeko zabwino pa maluso ndipo anapempha mtsogoleri  wa dziko kuti ayike ndondomeko zabwino kukonza malo owonetsela luso chifukwa ndi zomwe  Soldier ankafuna,

Iwo anawonjezera kuti zonse zokhudza nyimbo za Lucius zili m’malamulo ndipo tsopano zili m’manja mwa banja ndipo kuti oyimba ena pamene akuyimba popeleka ulemu kwa katswiriyu akuyenela kutsatabe malamulo.

Mlembi wa chipani cha United Transformation Movement (UTM) a Patricia Kaliati ati chiyambileni limodzi mu chipani chawo cha UTM m’chaka cha 2017, a Banda anali odzipeleka, okhulupilika komanso ndi amene anathandizira kubweretsa anthu ochuluka ku chipanichi.

A Kaliati ayamika mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera pokhala thandizo kwa Lucius Banda kuyambira pamene anayamba kudwala. Iwo ati dziko likulira kwambiri ndipo mwezi wa June wakhala mwezi owawa ku banja lawo la UTM komanso dziko lino.

“Tikupempheni a President a Chakwera, Lucius Banda wasiya mkazi ndi ana timati tikupempheni kuti  ngati nkotheka  kuwapezera ntchito kuti imfa ya bambo wawo isawawe”  a Kaliati anapempha.

Poyankhula Oyimilira mtsogoleri wa dziko lino yemwenso  ndi nduna ya za maboma ang’ono a Richard Chimwendo Banda, ati Lucius Banda anagwira ntchito modzipeleka  ndipo anathandizira ndondomeko zambiri za m’boma monga za NEEF, 

A Chimwendo Banda ati nyimbo za Lucius Banda  zinasunga ulaliki, utumiki, uneneli, kuyamika, chikondi ndipo zinalimbikitsa chikhalidwe m’dziko lino la Malawi.

Mfumu yayikulu Nsamala  ya M’boma la Balaka ati oyimba Banda anali msangalatsi wa boma la Balaka ndipo ati boma la a Chakwera liyesetse kupeza chakudya kwa anthu a mdela lake chifukwa kuli njala  popeza  dziko ndi boma lokoma ndi lomwe msilikali wa amphawi Lucius Banda  amkafuna.

Soldier Lucius Banda anamwalira pa 30 June mdziko la South Africa  atadwala nthenda ya Ipsyo kwa kanthawi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.