Chitetezo chili pa nsalu ya DPP basi: mtsikana adulidwa ziwalo, wina aphedwa ku DPP

Advertisement
Chikwawa

Pa ngodya zitatu za chipani cholamula cha DPP chija, imodzi ndiye ikukhala ngati ikuvutilapo. Anthu akugonabe ndi mantha, Chitetezo ndi kumpanda wachifumu kokha basi.

Anthu a mmudzi mwa Goma m’boma la Chikhwawa akukhala mwa mantha zigawenga zitapha ndi kudula mutu komanso ziwalo zobisika za mwana wina wa mmudzimo.

ChikwawaA Polisi ati Mayi wa mwanayo anamusiya ndi m’bale wake pa tsikulo iwo ndi kupita kukasaka ziwala.

Mmbuyomu ati kunabwela zigawenga zomwe zinapha mwanayo ndi kumuba, izo zinamudula mutu ndi ziwalo zobisika. Kenako zinakamuponya pa sukulu ya mmudzimo.

Pamene ku Nkhatabay, Apolisi ali pa kalikiliki osaka zigawenga zimene zidapha Bambo Levi Phiri a mmudzi mwa Nyambwani, Mfumu Yaikulu Fukamapiri.

Malinga ndi Apolisi, a Bambo Phiri adasowa kwa miyezi itatu koma kenako anadzaoneka pa 27 mwezi watha wa February ali chiledzelere.

Ako kadali komaliza iwo kuoneka ali moyo, kenako anapezeka ataphedwa.