Ophunzira yemwe wangomaliza maphunziro ake ku University ya Malawi (UNIMA) ku Zomba, wapha bwenzi lake lakale pomubaya ndi mpeni kwa Chikanda mu mzindawu.
Malingana ndi wachiwiri kwa wofalitsa nkhani pa polisi ya Zomba, Andrew Mwale, mnyamatayu ndi Raphael Kenala Liko yemwe akuganiziridwa kuti wapha Shingirai Mbenje wazaka 17.
Malipoti omwe tapeza akusonyeza kuti lachiwiri sabata ino, Shingirai pamodzi ndi mzake wina, amachokera mtauni ya mzindawu komwe mayi ake amagulitsa malonda.
Malipoti akuti atayandikila kufika pa malo ena otchedwa pa Tholo, Shingirai anadabwa kuwona Kenala Liko yemwe anasiyana naye chibwenzi pa kanthawi akumudikira.
Atakumanizana, Kenala Liko anauza malemuyu kuti ayendere limodzi poti anali ndi zoti akambirane naye zomwe Mbenje anakana.
Izi zinakwiyitsa mnyamatayu yemwe anayambe kumumenya mtsikanayu, mpaka kutulutsa mpeni ndikumubaya pa chifuwa kangapo.
Pakadali pano,male watsimikiza kuti Kenaka Lino ali m’manja mwa apolisi pomwe akuyembekezeka kukayankha mlandu wakupha munthu.

Killing a former friend out of jeoulosy is witchcraft. That person has no freedom and peace of mind among any community on earth,he must rot in jail
Some people are really wicked