
Timu ya mpira wa miyendo ya anyamata ya dziko lino ‘The Flames’ yafika tsopano mdziko muno kuchoka ku ulendo wake omwe inapita ku Tunisia kukasewera ndi timu ya dzikolo Lolemba komwe yakaswedwako 2-0.
Osewerawa afika mdziko muno kudzera pa bwalo la Ndenge la Chileka mu mzinda wa Blantyre ndi Kamuzu International mu mzinda wa Lilongwe komwe aliyense watsika malinga ndi komwe amakhala.
Osewera a Malawi anapita kukasewera ndi Tunisia yomwe ili patsogolo mu mndandanda wa gulu H ndi ma points 16 tsopano mu mpikisano odzigulira malo ku masewelo a pa dziko lonse a 2026 FIFA World cup qualifiers, masewelo omwe anachitika pa bwalo la Stade Olympique Hammadi Agrebi.
Mphunzitsi wa timu ya Malawi Kalisto Pasuwa anadandaulako kuti ma penate omwe anapelekelekedwa m’masewelo a Lolemba samayenera kukhala ma penate ndipo anati izo nzomwe zimachitika m’masewelo a mpira, ndipo akuyembekezera kuti akhale akuchita bwino mtsogolo muno.
Malawi inanyamuka kupita mdziko la Tunisia itagonga ndi Namibia 1-0 pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe, ndipo ku Tunisia Flames yafa 2-0 ndipo inaphonya penate yake mnthawi yakutha itha, komwenso Lloyd Aaron anatulutsidwa chifukwa cha nkhanza zina zomwe anachitira osewera mzake (red card)