Papa Francis awonekera ku gulu la anthu patatha sabata zisanu ali m’chipatala

Advertisement
Pope Francis, Head of the Catholic Church

Tsogoleri wa mpingo wa Chikatolika pa dziko lonse lapansi Papa Francis lero waonekera ndi kupereka moni ku khwimbi la anthu limene linasonkhana panja pa chipatala atagonekedwa kwa ma sabata asanu m’chipatalachi.

Malinga ndi nyumba zofalitsa nkhani m’dzikolo, Papa tsopano akupezako bwino ku nthenda ya Chibayo (Pneumonia) imene inakhudza mapapo onse awiri.

Poyankhula ku khwimbi la anthu limeme linasonkhana panja pa chipatalachi, Papa wathokoza madotolo amene adzipereka kugwira ntchito kuti iye apeze bwino komanso anthu osiyanasiyana amene akhala akumuikiza mapemphero.

Koma ngakhale izi zili chomwechi, umoyo wa Papa wachinambala 266 yemwe ali ndi zaka zakubadwa 88 ukanali wapendapenda ndipo patenga nthawi yaitali kuti thupi lake lichire bwino ku nthendayi.