
Sukulu ya Ukachenjede ya Malawi yachotsa ophunzira makumi awiri (20) kamba kochita zachinyengo m’mayeso.
Malinga ndi chikalata chomwe tsamba lino laona, ophunzirawa, omwe ndi a ma pulogilamu osiyanasiyana pasukulupa, anachita kusaweruzika pomwe amaonera, kukopera komanso kupanga mgwirizano wadala omwe ndiosaloledwa pa nthawi imene amapimidwa nzeru m’mayesomo.
Ophunzirawa, ataona kuti pachema, anaganiza zophwanya lamulo ndipo izi zawaika m’mavuto adzaoneni kamba kakuti asiyana nawo mkango umene umakhala pa pa pepala lomwe amatenga akamaliza sukulu (degree) yawo pamalo ochitira maphunzirowa.
Akulu akulu a sukuluyi atumizanso ku tchuthi chokakamiza ophunzira atatu kamba kongomatula mayankho nkuwasandutsa kukhala awo chonsecho sadalembe ndi iwowo.
Ophunzira m’modzi yekha ndi yemwe wapulumuka ku nkhondo ya angitawoyi pomwe wangopatsidwa chenjezo angakhale kuti nayenso anamupeza ndi mulandu ongomatula ntchito yoti siyake.
Izitu zatutumutsa ophunzira ambiri pasukulupa omwe adziwiratu kuti moto, umapita kumene kwatsala tchire.