Njatani onse onena kuti Chilima anaphedwa – yatelo Komishoni

Advertisement
Saulos Chilima

Bungwe la padera lomwe linakhazikitsidwa kuti lifufuze za ngozi yomwe idapha wachiwiri wakale kwa mtsogoleri wa dziko lino yapempha apolisi kuti athane ndi onse ofalitsa nkhani zomwe ati ndi zabodza pa masamba a mchezo.

Mu mfundo imodzi yomwe iwo amanga ataunika umboni okhudza ngoziyi, iwo ati apolisi akuyenera kuthana ndi kufalitsidwa kwa nkhani zabodza zokhudza ngoziyi.

Malinga ndi bungweli lomwe linakhazikitsidwa ndi mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera a mabungwe ataopseza kuchita zionetsero, ati pamene kunachitika ngoziyi kunavumbuluka nkhani zambiri. Ati zina ndi zabodza.

“Imodzi mwa mfundo imene tingapemphe ndi yoti apolisi alimbane ndi onse ofalitsa nkhani zabodza maka pa masamba a mchezo,” anatero mmodzi mwa ma Komishonala a bungweli.

Iwo alandulanso kuti apolisi akuyenera kusakasaka angoni amene amachita zionetsero za mkwiyo ndi imfa ya a Chilima mpaka kutseka mseu.

“Tikupempha apolisi kuti awasake anthu amenewa ndipo athane nawo,” anatelo a bungweli.

Iwonso alamula kuti apolisi afufuzane kuti amudziwe amene adagawa zithunzi zoonetsa malo angoziwa zimene mwa zina zinaonetsa malemu a Chilima atavulidwa zovala.

“Mukufufuza kwathu taona kuti Zithunzi izi zidatulutsidwa ndi a polisi, amusake adazitulutsayo ndipo amulange,” anaonjezeranso pamenepo.

A bungweli ati mukufufuza kwawo apeza kuti a Chilima sanaphedwe monga ena amaganizira koma kuti idali ngozi basi.

A Widow’s Plea: Mary Chilima seeks truth behind husband’s tragic death

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.