Mwambo wa nsembe ya Misa olemekeza malemu Kanyongolo wachitika

Advertisement
Kanyongolo

Mwambo wa nsembe ya Misa opereka ulemu komanso opemphelera Malemu mayi Ngeyi Kanyongolo unachitikira pa mpingo wa Zomba mu dayosisi ya Zomba ndipo unatsogozedwa ndi Bishop Alfred Mateyu Chaima mothandizana ndi Archbishop Thomas Luke Msusa wa Dayosisi ya Blantyre.

Kumwambowu kunafikanso mtsogoleri wakale wadziko lino a Joyce Banda pamodzi ndi Mkulu wakale wazamalamulo Richard Banda.

Poyankhula pamwambowo, a Chaima anayamikira malemuwa chifukwa chokhulupilira Mulungu moyo wawo onse.

Iwo anati ngakhale iwo adali munthu ophunzira kwambiri komanso kugwira ntchito zapamwamba, a Kanyongolo adali odziwa kucheza ndi wina aliyense posatengera maphunziro awo.

Iwo anaonjezera ponena kuti moyo wa malemuwa wapindulira akhristu ambiri mu dayosisi ya Zomba ngakhalenso ma dayosisi ena onse M’malawi muno.

A Chaima anatinso bungwe la chizimayi la mpingo wa Katolika la Catholic Women ku Zomba limayenda bwino chifukwa cha upangili wa wa mayi Kanyongolo omwenso amathandiza kayendetsedwe kosiyanasiyana pogwiritsa ntchito chuma chawo.

Iwo anapereka uthenga opepesa kubanja la a Edge Kanyongolo kuti asataye mtima koma ayike chikhulupiliro chawo mwa Mulungu.

“Tiwasowa Mayi Kanyongolo chifukwa cha zintchito zawo zabwino zomwe amachita pothandiza mpingo kuno ku Zomba ndipo ndipemphe Ansembe kuti mukamachita mapemphero muziwapemphelera malemuwa,” iwo anayankhura motero.

Poyankhulanso, Wapampando woyimilira akhristu onse a Zomba Diocese a Edward Kalemba anati imfa ya mayi Kanyongolo yadzidzimutsa anthu ambiri ndipo mpingo wataya munthu ofunika kwambiri yemwe amathandiza munjira zosiyanasiyana.

Iwo anati malemu Kanyongolo anali ndi mphatso yothandidza anthu osowa ngakhalenso kulipilira ana amasiye sukulu ndipo adapempha akhristu kuti atengere chisanzo chawo cha ntchito zabwino.

Thupi lamalemuwa lilowa m’manda Lachinayi osati Lachitatu monga momwe adalengezera poyamba ndipo likayikidwa kumudzi kwawo kwa Che Chamba, T/A Bvumbwe Boma la Thyolo.

Malemu Kanyongolo adamwalira lolemba pa 28 October pa chipatala cha Mwai Wathu atadwala nthawi yochepa ndipo amamwalira ali Wachiwiri wamkulu oyendetsa sukulu ya ukachenjede ya mpingo wa Katolika (Catholic University).

Advertisement