Titulitsireni ng’anga yathu, amang’ara anthu ku Mzimba

Advertisement
Malawi24

Khamu la anthu ochokera m’mudzi wa Mujinge mfumu yayikulu M’mbelwa m’boma la Mzimba lakhamukira ku polisi ya Mzimba komwe akufuna kuti a polisi atulutse sing’anga wawo yemwe akuti amachotsa ufuti mwa anthu m’mudzimo.

Sing’angayo yemwe akudziwika kuti Nyauzimu Gondwe akuti anachokera m’boma la Rumphi  kubwera m’mudzi wa Mujinge atayitanidwa ndi anthu  limodzi ndi mafumu a mudzimo kuti adzasese mudzi.

Apolisi amanga sing’angayo atatsinidwa khutu ndi anthu ena kuti m’mudzi mwa Mujinge sikulibwino pomwe sing’anga akugumula ziliza kuti achotse nyanga.

Pakadalipano anthu okonda sing’angayo ali kunja kwa polisi ya Mzimba kudikira apolisi kuti atulutse sing’anga wawoyo.

M’neneri wa polisi ya Mzimba Peter Botha watsimikiza za kumangidwa kwa sing’angayo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.