Chipani cha Umodzi chasankha mtsogoleri watsopano

Advertisement
Umodzi Party

Nthumwi ku msonkhano waukulu wa chipani cha Umodzi Party (UP) zasankha mtsogoleri watsopano yemwe akuyembekezeleka kugwira ntchito yawo kwa zaka zisanu. 

Pa msonkhano omwe udachitikira ku Robin’s Park Lamulungu mu mzinda wa Blantyre, a Thomas Kaumba asankhidwa kukhala mtsogoleri watsopano wa chipanichi atagonjetsa a Mary Piyasi ndi mavoti 59 kwa 29.

Thomas Kaumba
Thomas Kaumba the newly elected Umodzi Party leader.

Poyankhula atasankhidwa pa udindowu, a Kaumba ati agwira ntchito mwamphamvu komanso modzipereka ndipo awonetsetsa kuti chipani chawo chidzakwanitse kupeza mipando ya ma khansala komanso aphungu kunyumba ya malamulo mu zisankho za chaka cha mawa.

Iwo alowa m’malo mwa Professor John Chisi omwe adatuluka mu chipanichi mu mwezi wa November chaka chatha ndipo padakalipano ndi membala wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP).

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.