Kampani zopanga sugar zikuzunza a Malawi – CDEDI

Advertisement
CDEDI says Malawi not benefiting from Malawian Airlines, Greenbelt Authority

Bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI), lati Kampani zopanga sugar za Illovo ndi Salima zikuzunza a Malawi pokweza mitengo ya sugar amenenso sakupezeka pa msika.

Poyankhura pa msonkhano wa atolankhani omwe bungweli lidachititsa lachiwiri ku Lilongwe , mkulu wa bungweli a Sylvester Namiwa ati kukwera kwa mitengoku kwabweretsa poyera m’chitidwe wa ukathyali ndi nkhanza zomwe kampanizi zikuchitira a Malawi.

A Namiwa ati bungweli likudabwa ngati aliponso munthu m’boma yemwe akuwaganizira a Malawi omwe akudutsa mu nyengo zowawa pa nkhani ya zachuma.

Iwo anawonjezera ponena kuti a Malawi ndi okhumudwa ndi nduna ya za malonda, a Sosten Gwengwe, omwe pansi pa unduna wao, kampani za sugar  zikungopanga ziganizo zokomera iwo okha.

“Kukwera kwa mitengo ya sugar kukugwirizana ndi zomwe bungwe la CDEDI lidanena kuti kampanizi zinachita kupangira dala kuti sugar asowe, kenako anthu akamadzavutika, iwo adzabweretse sugar koma pa mtengo okomera iwowo osati a Malawi,” a Namiwa anafotokoza.

A Namiwa anapitiliza ponena kuti kampani ya Illovo imayenera kuyamba kaye yabweretsa sugar pamsika isanakweze mtengo.

Iwo anawonjezera ponena kuti zomwe apanga ma kampani a Illovo ndi Salima zikupangitsa bungweli kukaikira kuti boma likuthandizira kampanizi kuti lisamagwiritse ntchito malamulo omwe amayenera kuteteza a Malawi.

 “A Malawi akukumbukira bwino kuti mu August 2023, kampani ya Illovo inakatenga chiletso kuletsa unduna wa za malonda ndi ma fakitale kutsitsa mtengo wa sugar ndi 25 kwacha pa 100 kwacha iliyonse, ndipo mbali inayi, kuletsanso mkulu ozenga milandu ya boma, Director of Public Prosecutions, kuti asazenge milandu kampaniyi Kamba kopanga malonda mosatsata malamulo a Competition and Fair-Trading Act “, Anamiwa anatero.

Iwo apempha  mkulu oimila boma pa milandu, a Thabo Chakaka-Nyirenda, kuti alowelelepo mwa changu pa nkhaniyi potengera kuti meyizi isanu ndi iwiri yapitayo anawapemphanso pa nkhani yomweyi ndiponso ati  nyumba ya malamulo itulutse lipoti lokhudza nkhani ya mitengo ya sugar yomwe inachitika mu July 2023, ndi komiti ya nyumba ya malamulo yoona za malonda.

Bungwe la CDEDI lati likufuna mkulu wa zokambirana m’nyumba ya za malamuro a Richard Chimwendo Banda kuti afotokoze kuti n’chifukwa chiyani nyumba ya malamulo sinavomereze lipoti la komitiyo, m’mikumano yake iwiri yapitayi.

Powonjezera apo, ati  nduna ya za malimidwe a Sam Kawale afotokozere a Malawi, chomwe chikuchedwetsa kuti apeleke ku nyumba ya malamulo, bilu yokhudza za sugar, yomwe ili ndi kuthekera koteteza a Malawi ku nkhanza zomwe kampani za sugar zi zikuchitira anthu mdziko muno, komanso kuthandiza kubweretsa ndalama za kunja.

A Namiwa ati a Malawi akudikira ndi chidwi kuti amve kuchokera kwa Attorney General za tsogolo la Salima Sugar Company, yomwe inakhazikitsidwa kuti iteteze anthu pobweretsa mpikisano wabwino pa malonda a sugar.

Pomaliza awuza kampani za Illovo ndi Salima sugar kuti ziyambe zaimitsa kaye kukweza mitengoku, kufikira pomwe sugar adzayambe kupezeka ponse ponse m’dziko muno.

Advertisement