Kuno ayi ti anthu ta katangale inu – dziko la USA lauza a Matemba ndi ena kuti asazapitenso ku Amereka

Advertisement
Malawi Corruption

Ngati sanapiteko ndi komwe ndiye nyimbo ya Buffalo Soldier ya a Gidess Chalamanda asiya kumvera. Koma ngati anapondako kale ati asazabwelerekonso. Dziko la United States of America lalengeza kuti ena mwa adindo a dziko lino asadzapitekonso ati kamba ali ndi chifungo cha katangale.

Izi zili mu kalata imene dzikoli latulutsa lero. Malinga ndi kalatayi, amene anali mkulu olimbana ndi katangale a Matthews Matemba ndinso Mayi a kunyumba kwawo ati asadzayerekeze ndi komwe kuponda dziko la Amereka. Ati chifukwa mkuluyi analandira ziphuphu kwa mkulu wina wa za malonda, amene anthu akuganizira kuti ndi a Zuneth Sattar.

Kuphatikizapo a Matemba ndi akazi awo, dziko la Amereka lati naye mkulu oyimila anthu pa milandu amene anakhalapo mtsogoleri wa bungwe la ma loya, a John Suzi Banda nawonso asazaonetse chipumi mu dziko la Amereka. Iwowa aletsedwanso pamodzi ndi Mayi a kunyumba kwawo.

Naye mkulu wakale wa polisi, a George Kainja amuletsa kukaponda ku Amereka. Nkhani yake ndi yakatangale yomweyi. Iyeyu, limodzi ndi a kumphasa kwake, awaletsera limodzi.

A dziko la Amereka auzanso bambo Mwabi Kaluba amene ndi loya wa a Polisi mu dziko muno kuti iye limodzi ndi a kunyumba kwake asazayerekeze kuponda dziko lawo.

Dziko la Amereka lati lachita izi potsatira kuononga kwa mchitidwe wa katangale mu dziko muno, ndipo lati abambo anayiwa akukhala ngati za udindo wawo anayiwalilatu koma kusangalatsa bambo Sattar basi.

Nkhani za katangale zamanga nthenje mu dziko muno pamene sabata latha lomweli mtolankhani wathu wakale ananjatidwa ndi a polisi chifukwa choulula kuti mkulu wina oganiziridwa za u kamberembere ndi katangale, a Batatawala, akupitiriza kusolola ndi boma la Chakwera

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.