Ofesi ya Zaumoyo ikufufuza za anthu omwe afa ku Blantyre

Advertisement

Ofesi ya Zaumoyo m’boma la Blantyre yati ikufufuza za imfa ya anthu asanu omwe amwalira kutsatira atamwa mowa osadziwika bwino ndipo ofesiyi yati idzabweretsa poyera zotsatira zakafukufuku-yi akatha.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe khonsolo ya mzinda wa Blantyre yatulutsa ndipo wasayinira ndi mkulu wa za umoyo a Dr. Gift Kawalazira.

Kudzera mkalatayi ofesiyi yati yalandira malipoti oti anthu okwana asanu amwalira kutsatira atamwa mowawo

Pakadali pano ogwira ntchito zachipatala akufufuza zomwe zachitikazi ndipo zotsatira zake zidzaperekedwa poyera.

Kafukufuku akuonetsanso kuti anthu ena awiri adagonekedwanso pa chikalata cha Queen Elizabeth atamwa mowawu.

Advertisement