Magetsi ayambiranso kuvuta m’boma la Mzimba

Advertisement

Magetsi ayambilanso kuvuta ku boma la Mzimba komwe anthu ayamba kukhalaso maola wochuluka kopanda magesi.

Miyezi ingapo yapitayi, magetsi amavutanso zomwe zinapangitsa amabungwe komanso ochita malonda kudzuzula bungwe la ESCOM kamba kosalabadila kuwapatsa magezi.

Mwezi watha, nduna yowona zamphamvu za magesi a Ibrahim Matola inakayendera ofesi ya Escom ya boma la Mzimba ndipo akuluakulu a bungweli nawo anali ndi mkumano ndi anthu wochita malonda, amabungwe limodzi ndi ena wokhuzidwa.

Chichokeleni mkumanowo womwe unachitika mwezi wa January, magetsi akhala asakuvuta ndipo anthu anayamba kuyiwala zakuvuta kwa magesi.

Koma pakali pano anthu m’bomali ayamba kukumanso ndi vuto la magesi.

Kukumveka mphekesera kuti laini yomwe ikupereka magetsi ku Mzimba pa boma kuchokera pa Transformer ya pa Chikangawa akumayisitha kuyipititsa ku laini yomwe ikupereka magetsi ku Lundazi, pazifukwa zomwe akuti Ku Lundazi kwatsegulidwa ma kampani ambiri womwe akufuna mphavu ya magesi wochuluka.

Ngati njira imodzi yosangalatsira eni amakampani a ku Lundazi ku Zambia, akuti akuyenera kumazimitsa laini ya ku Mzimba boma.

Bungwe la Escom lapempha nthawi kuti liyankhepo pa nkhaniyi.

Advertisement