Asilikali apulumutsa nawo anthu ku Dwangwa

Advertisement

Asilikali a dziko lino atenga nawo gawo populumutsa anthu pafupipafupi 200 omwe akhudzidwa ndi madzi osefukira ku Dwangwa m’boma la Nkhotakota.

Malingana ndi lipoti lochokera ku khonsolo la Nkhotakota, asilikaliwa akugwiritsa ntchito mabwato awo apa madzi kupulumutsa anthuwa. Pafupipafupi anthu okwana 6,145 ndi amene akhudzidwa kwambiri ndi madziwa.

Malingana ndi chiwerengero chomwe khonsolo ya bomali yatulutsa, ena mwa anthuwa, omwe ndi okwana 4985, ndi anthu a m’dera la mfumu yaikulu Kanyenda pamene anthu 957 ndi ochokera kwa mfumu yaikulu Mponde ndipo 67 ndi ochokera dera la yaikulu Malenga.

Pakanali, pano misasa yomwe yamangidwa ikusunga anthu pafupipafupi 6,000.

“M’modzi mwa anthu amene anali mu bwato lopulumutsa anthu wamwalira pamene bwato limene anakwera linatembenuzika. Miseu yaduka ndipo tili ndi vuto lalikulu limene likupangitsa kuti kukhalale kovuta kufikira anthu amene akhudzidwa kwambiri ndi vutoli,” watero mkulu ofalitsa nkhani m’boma la Nkhotakota.

Iwo anapitiriza kunena kuti thandizo la ndalama komanso zinthu zonse zofunikira pa moyo wa munthu zikufunikira kwambiri kwa anthu omwe akhudzidwa ndi vutoli m’bomalo.

Advertisement