Chimanga chovuta kale a Khonsolo achitchetcha cha nthete

Advertisement

Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe yati yatchetcha minda Khumi (10) ya chimanga chifukwa cholima mbewuzi m’malo oletsedwa.

Khonsoloyi kudzela ku mbali yokhwimitsa lamulo ati dongosolo lotchetcha chimanga ndi mbewu zina zomwe anthu analima m’malo osaloledwa likhala likupitilira.

Malingana ndi wamkulu wa okhwimitsa malamulo mu khonsoloyi a Allan Domingo ati ayamba ndi madela a ku 43 lachiwili pa 27 February 2024 kumenenso ambiri adadzala m’malo osaloledwa ndipo akhala akulowera madela ena.

A Domingo ati iwo akutchetcha motsatila malamulo kamba kakuti anthuwa akuphwanya malamulo a Physical Planning a mchaka cha 2018 omwe amati kugwiritsa ntchito malo ongokhala, a mbali mwa msewu kudzalapo mbewu mopanda chilolezo mkoletsedwa.

Khonsolo ya mzindawu m’mawu ake pa tsamba lawo la mchezo apempha anthu kuti nthawi zonse azitsalira malamulo ang’ono a mzindawu.

Chimangachi chikutchetchedwa chokulakula pamene dziko lino lili pa chiopsezo cha njala yogonela kamba ka ng’amba yomwe yakuta dziko lino kuphatikizapo mayiko ena ozungulira.

Funso mkumati Kodi khonsolo imadikira chikule chibeleke tiwana kuti akatchetcha anuwake a mbewuzi alire mokweza kuti likhale phunzilo kwa Iwo?.

Advertisement