Bambo wina wadzikhweza ku Dowa

Advertisement
Suicide

Bambo wina ku Dowa  yemwe dzina lake ndi Kelvin Songazaudzu wa zaka 47 zakubadwa wadzimangilira kudenga la nyumba yake kaamba kamavuto a m’banja.

Mneneri wa apolisi m’bomali a MacPatson Msadala watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati malemuwa ndi a m’mudzi wa Chimphapa m’dera la mfumu yayikulu Chakhaza ku Dowa komweko.

Malingana ndi a Msadala, bamboyu wakhala akukumana ndi mavuto am’banja kuyambira chaka chatha pamene iye wakhala akumuganizia mkazi wakeyo kuti amayenda chanseri ndi amuna ena.

Ndipo apolisi anapezanso mankhwala ozunguza bongo a Cuba pafupi ndi thupi lamalemuyo omwe akuganizilidwa kuti malemuwa anagwilitsa ntchito.

Achipatala atapima thupi la malemuyu anapeza kuti iye wamwalira kamba kobanika komanso kufooka kwambili.

Advertisement