Alimi a Zomba Malosa adandaula kuti sadagulebe fetereza wobereketsa

Advertisement
Malawi Farmers

Alimi a mdera la Zomba Malosa adandaula kuti mpaka pano sadagulebe fetereza wobereketsa wa Urea ndipo awopseza kuti pofika lachiwiri ngati akhale asadagule achita chothekera kuti akafike kumalo omwe amapangira fetereza ndikukachita ziwonetsero.

M’modzi mwa alimi ochokera mdera la Zomba Malosa a Lanjesi Saizi auza Malawi24 kuti tsopano chikhulupiliro chawathera chokuti akhala ndi mwai ogula fertilizer wa Urea popeza tsopano nthawi ikupita kokutha komanso chimanga chikukula.

A Saizi ati pakali pano adakandaula nkhaniyi kwa Phungu wamdera la Zomba Malosa Wolemekedzeka Mai Grace Kwelepeta ndipo apempha phunguyu kuti adzawaperekedze kumalo omwe amapangira fetereza kuti akapereke madandaulo awo.

Iwo ati ngati alimi amdera la Zomba Malosa angalephere kugula fetereza wobereketsa ndiye kuti apitilirabe kuvutika ndi njala chaka chino popeza mdelari kuli njala yadzawoneni.

‘Tipemphe unduna wazamalimidwe kuti utiganizire ife anthu a kuno ku Zomba Malosa potibweretsera fetereza wa Urea popeza chiyambireni palibe yemwe wagula,” adadandaula motero a Lanjesi Saizi.

Malawi24 idayetsetsa kuyankhula ndi Phungu wamdera la Zomba Malosa Mai Grace Kwelepeta ndipo adatsimikiza kuti anthu a mdera lawo  sadagulebe fetereza wobereketsa wa Urea zomwe zikuyika pachiwopsezo kuti alimi avutikabe ndi njala.

Mai Kwelepeta ati adayetsetsa kufuna kuti akumane ndi Nduna yazamalimidwe kuti ayifotokezere zavutoli koma izi zidalephereka.

Phunguyu watsimikizilanso kuti alimi amdera lawo adawapeza ndikuwapempha kuti adzawaperekeze kumalo omwe amapangira fertilizer kuti akapereke nkhawa zawo ndipo phunguyu wamvomera kuti aliwokodzeka kuwaperekedza.

Advertisement