Phungu watsekulira chipinda chophunziliramo m’dera lake


Phungu wa nyumba ya malamulo mchigawo chapakati m’boma la Salima watsekulira chipinda chophunziliramo ndi kupereka mayunifolomu kwa ophunzira okwana 100 pa sukulu yapulayimale ya Demera yomwe ili mdera la mfumu yayikulu Maganga m’bomali.

Malingana ndi Phunguyi, a Kapisen Phiri, wati wamanga chipinda chophunziliramochi kaamba koti pasukuluyi padalibe zipinda zophunzililaramo zokwanira.

Chipindachi chamangidwa ndi thandizo lochokera ku CDF. Kuphatikizapo apo a Kapisen Phiri, aperekanso masukulu Unifolomu kwa ophunzira 100 pofuna kuonetsetsa kuti  mwana aliyense ali ndi mwayi opeza maphunziro mdera lake.

Mphunzitsi wamkulu pa sukuluyi Anord Kasambala anayamikira Phunguyi  pazomwe wachita pa sukuluyi ponena kuti mavuto omwe amakumana nawo maka mu nyengo ya Dzinja achepa komaso Maunifolomu omwe wapeleka anthandizira kuti ophunzira akhale ndi chidwi pa maphunziro awo.

Nayo mfumu yayikulu Maganga yomwe inali nawo pa mwambo otsekulira chipindachi yati ndi yosangalala kamba ka chitukukochi. Kotero ati achita chothera kuti anthu amdera lake akusamalira chitukukochi.