Bwalo lamilandu lalamula mamuna ochita zamathanyula kukakhala kundende zaka 8


Bwalo la milandu ku Zomba lalamula mamuna wina Andrea Nkula Masamba kuti akagwire ukaidi wakalavula gaga ku ndende kwa miyezi zaka 8 chifukwa chomupeza olakwa pamulandu ochita zamathanyula.

Wapolisi oyimira Boma pamilandu Sub-Inspector Evelyn Dzoole adapempha bwalo kuti lipereke chilango chokhwima kwa Masamba chifukwa zomwe adachita pogonana ndi mamuna nzake ndizosemphana ndi malamulo a dziko lino komanso kuti anthu ena amtima ngati umenewu atengerepo phunziro.

Andrea Masamba adapalamula mulanduwu mwezi wa March chaka chino ndipo adapempha bwalo kuti lisamupatse chilango chokhwima popeza kupalamula uku ndikoyamba.

Koma popereka chigamulo chake, Chief Resident Magistrate Austin Banda adagwirizana ndi wapolisi oyimira Boma pamilandu kuti a Masamba ayenera kuti alandire chilango chokhwima popeza zomwe adachita ndizosemphana ndi malamulo oyendetsera mdziko lino.

Pamenepa, Chief Resident Magistrate Banda adagamula kuti a Masamba akhale ku ndende ndikukagwira ukaidi wakalavula gaga kwa miyezi 96 (zaka 8).

Andrea Nkula Masamba ali ndi zaka 25 zakubadwa ndipo amachokera mudzi mwa Njala mdera la T/A Nkagula Boma la Zomba.