Boma lati lagula mathalakitala 8 oti athandize ulimi wa m’ma Mega Farm


Minister of Agriculture Malawi

Boma lati lagula mathalakitala asanu ndi atatu omwe agawidwe mzigawo za chitutuko cha ulimi mdziko muno (ma ADD) ndi cholinga cholimbikitsa ulimi wa ma Mega Farm.

Nduna ya zamalimidwe a Sam Kawale atsimikiza izi pa msokhano wa atolankhani ku Lilongwe.

A Kawale ati mathalakitalawa athandiza alimi m’dziko muno kulima malo aakulu pogwiritsa ntchito makina ndipo izi zithandizanso kuti azilima mwachangu ndi kumakolola zochuluka.

Iwo anatinso ku ma ADD komwe mathalakitala wa agawidwe, alimi owe akuchita ulimi wa ma Mega Farm azitha kukabwereka.

Ndunayi inawonjezera kuti Boma lalandiranso makina ogwiritsa ntchito pokolola mbewu (combine harvester) kuchokera ku Boma la dziko la China.