Kupweteka kwa Thandi Galeta kunatisokoneza, watero mphunzitsi wa Malawi

Advertisement

Mphunzitsi wa timu ya mpira wa manja ya Malawi Samuel Kanyenda wati kupweteka kwa Thandi Galeta kunasokoneza timuyi lero pa masewera ake ndi Uganda.

Uganda yasambwadza Malawi ndi zigoli 57 kwa 46 lero masanawa mu chikho cha dziko lonse lapansi cha Netball World Cup ku South Africa.

Poyankhula mpirawu utatha, Kanyenda anati Malawi zayivuta lero chifukwa Galeta anapweteka.

A Kanyenda anati matimuwa anafanana zigoli mu kota youamba koma zinthu zinavuta mu kota yachiwiri pomwe Galeta anavulala.

“Galeta anatulutsidwa koma zinakhala ngati tadzidzikutsidwa ndiye zinthu zinasokonokera pamenepo,” anatero Kanyenda.

Kutsatira kuluza kwa lero, Malawi singakhalenso pa nambala 5 ku mpikisanowu ndipo izamenya masewera ake omaliza lamulungu omwe ndi olimbirana nambala 7.

A Kanyenda ati osewera a Malawi ndi okonzeka kuzapambana pamasewero amenewa.

Iwo anaonjezera kunena kuti Malawi ikufunikanso isakesake osewera ena achisodzera usanafike mpikisano wina wa dziko lonse lapansi pazakhale timu.

Advertisement