Okhudzidwa ndi Namondwe Freddy alimbikitsidwa kuchita ulimi wamthilira

Advertisement

Ngati njira imodzi yochepetsera mavuto omwe anthu omwe anakhuzidwa ndi namondwe wa Freddy akukumana nawo, bungwe la Child Focus likulimbikitsa anthu okhala m’mudzi wa Sambazi, mfumu yaikulu Phimbi m’boma la Balaka kuchita ulimi wamthilira.

Monga mmene zidakhalira mmadera ena a mchigawo cha kummwera kwa dziko la Malawi, namondwe wa Freddy adawononga katundu osiyanasiyana monga nyumba,misewu komanso  kukololora mbewu zosiyanasiyana m’minda ya anthu zomwe zidapangitsa kuti akhale pa mavuto adzaoneni monga kusowa malo okhala komanso chakudya.

A Winnie Bishop omwe ndi m’modzi mwa anthu omwe adakhuzidwa ndi namondweyu ati moyo udali ovuta kwambiri potengera kuti adataya katundu osiyanasiyana ofunikira omwe amkadalira pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku zomwe zidapangitsa kukhala opanda chiyembekezo.

”Moyo udali olimba kwambiri chifukwa timasowa mtengo ogwira,” adatero a Bishop.

Mai Bishop omwe adakhalaponso mkulu oyang’anira anzawo pa msasa omwe udali pa tchalitchi cha Sambazi Living Waters ati ngakhale anthuwa amalandira thandizo la chakudya komanso zinthu zina zosiyanasiyana kuchokera ku mabungwe osiyanasiyana, thandizoli silimathetselatu mavuto awo onse kaamba kakuti limakhala la nthawi yochepa chabe.

Iwo adati bungwe la Child Focus lawathandiza kuti ayambenso kudzidalira paokha kudzera mu ntchito ya ulimi wamthilira.

”Padakalipano, mbeu za kumunda zomwe tidabzala monga chimanga komanso mbatata zikukula bwino ndipo tili ndi chiyembekezo chachikulu kuti posachedwapa tikolora chakudya chokwanira,” adafotokoza motero Bishop.

Bungwe la Child Focus lidathandiza maanjawa ndi zipangizo za ulimi monga feteleza, mbeu ya chimanga komanso mbatata kuphatikizaponso katundu osiyanasiyana monga ufa, mafuta ophikira, soya pieces, mchere komanso sopo.

Mkulu wa bungwe la Child Focus a Thomas Sendeza ati bungwe lawo  ndi lokhutira ndi mmene anthuwa akudzipelekera pa ntchito ya ulimi ndipo atsindika kuti ndi cholinga cha bungwe lawo kuti lithandizile kuchepetsa umphawi omwe udadza kamba ka namondwe wa Freddy.

Maanja okwana 31 akulima pa sikimu yomwe kukula kwake ndi hekitala imodzi ndi theka.

Bungwe la Child Focus likugwira ntchitoyi ndi chithandizo cha ndalama kuchokera ku bungwe la World Connect Malawi.

Advertisement