Red Lions komanso Civo alepherana ku Balaka

Advertisement

Pamene matimu a mpira wa miyendo ali palikiliki kusaka chipambano mu mpikisano wa 2023 TNM ipatse moto, ma timu a Red Lions komanso Civo Service United masana a lero alepherana pogoletsana chigoli chimodzi aliyense.

Timu ya Civo ndi yomwe idayamba kupeza chigoli kudzera mwa Lovemore Mbeta yemwe anagoletsa mu mphindi 66 mchigawo chachiwiri.

Komabe, Civo yomwe idayaka moto kuchokera kumayambiliro a masewero idakanika kuteteza golo lawo, zomwe zidapangitsa kuti asilikali a ku Zomba athire nkhondo mu ukonde wa Civo mu mphindi 80 mchigawo chachiwirichi kudzera mwa Ferguson Mtondo.

Poyankhula ndi Malawi24 pakutha pa masewero, othandizira mphunzitsi wa timu ya Red Lions, Chifundo Masapula adali okondwa ndi zotsatira za masewerowa.

”Ndine osangalala kwambiri kuti takwanitsa kubweza chigoli ngakhale kuti ichi sichinali cholinga chathu kuti tifanane mphamvu ndi timu ya Civo.Komabe, tikudziwa kuti chilichonse chimachitika pa masewero,” anatero Masapula.

Ndipo m’mawu ake, Wilson Chidati yemwe ndi mphunzitsi wa timu ya Civo anati ndi okhutira ndi m’mene anyamata ake anasewelera masewero ngakhale kuti sadathe kupeza chipambano.

Iye adawonjezera kunena kuti anyamata ake anakanika kugwilitsa ntchito mipata yomwetsa chigoli yomwe adapeza.

”Vuto lathu lalikulu ndi lakuti tinaphonya mipata ingapo yomwe anyamata adapeza komabe tiyesetsa kukonza vutoli,” anafotokoza Chidati.

Pamapeto pa zonse, osewera wa Civo, Timothy Sulwimba ndi yemwe adasankhidwa kukhala osewera yemwe adasewera kuposa anzake onse.

Follow us on Twitter:

Advertisement