Ogwira ntchito za Boma ku Balaka alonjezedwa kulandira malipiro awo lero

Advertisement

Bwanamkubwa wa boma la Balaka, Darwin Mngoli, wati anthu ogwira ntchito mu nthambi zosiyanasiyana za boma mu khonsolo ya Balaka alandira malipiro awo a mwezi wa May pakutha pa tsiku la lero, lolemba pa 5 June 2023.

A Mngoli anena izi pakutha pa mkumano omwe adali nawo ndi nthumwi zoyimira ogwira ntchito za boma pa bomali komanso akuluakulu ena a khonsolo ya Balaka.

Kum’mawaku, ogwira ntchitowa omwe ndi kuphatikizapo aphunzitsi, ogwira ntchito za umoyo komanso ena ambiri adakhamukira ku ma ofesi a khonsolo-yi ati kukawonetsa kusakondwa kwawo ndi kuchedwa kwa kulandira malipiro awo.

Poyankhulapo pa za vutoli, a Mngoli adafotokoza kuti izi zidachitika malingana ndi kuchepa kwa ndalama zomwe khonsolo-yi idalandira kuti ikonzere malipiro a ogwira ntchitowa.

”Tidalandira ndalama zoti titha kukonzera malipiro koma tidazindikira kuti ndalama zidali zosakwanira.

”Titalongosola za vutoli ku likulu tidalandiranso uthenga wakuti titha kupitiliza kupanga ma votcha a malipiro koma tili mkatikati opanga izi zidapezekanso kuti padapezekanso mavuto ena,” adalongosola motero a Mngoli.

Poyankhula ndi Malawi24 ku m’mawaku, m’modzi mwa ogwira ntchitowa a Patricia Chimwala omwe ndi mphunzitsi pa sukulu ya Pulaimale ya Bazale adati kuchedwa kwa kulandira malipiro awo kukupangitsa moyo kukhala olimba kwambiri ati kamba kakuti akusowa mtengo ogwira.

”Kodi tingagwire bwanji ntchito tili ndi njala?” adafunsa motero a Chimwala.

Follow us on Twitter:

Advertisement