Mwana wakhanda wapezeka atafa mumtsinje wa Likangala

Advertisement

Mwana wakhanda wamiyezi yosachepera itatu yemwe mai ake sakudziwika wapezeka atafa mumtsinje wa Likangala mu Mzinda wa Zomba.

A Auzious Chimalala omwe amakhala m’mudzi mwa Chilupsa mu Mzinda wa Zomba awuza Malawi24 kuti ana ena omwe amakasamba mumtsinje wa Likangala ndiwomwe adamupeza mwanayu alimu Jumbo yokuda ya pulasitiki ataponyedwa m’madzi.

A Chimala ati izi zitangochitika anthu ozungilira mderali adakadziwitsa apolisi zankhaniyi kuti afufuze mwini wake wamwanayo.

Iwo ati akukhulupilira kuti Mai wamwanayu apezeka ndipo ati aka ndikoyamba kuti zinthu ngati izi zichitike mdelaro.

Mai wina yemwe sadafune kuti timutchule dzina adati ndizomvetsa chisoni kupha mwana wobereka wekha ndipo wapempha a polisi kuti Mai amene wachita izi akapedzeka akandire chilango chokhwima.

Pakali pano apolisi ku Zomba sadayankhulepo kanthu zankhaniyi.

Follow us on Twitter:

Advertisement