Musadzabwerenso ndi ziphuphu kuno, yatero nthambi ya DRTSS

Advertisement

Nthambi yowona za pamsewu ya Directorate of Road Traffic and Safety Services (DRTSS) yaletsa anthu kuti asamapiteso kuma ofesi awo ndi ziphuphu ponena kuti nthambiyi ndiyosinthika tsopano.

Izi ndi malingana ndi chithunzi cha chikwangwani chomwe chikuoneka kuti chaikidwa kuma ofesi a nthambi ya DRTSS chomwe pano anthu akugawana m’masamba a mchezo.

Pachithuzichi palembedwa mawu oletsa anthu kupita ku ma ofesi a nthambiyi ndi ndalama zomwe amaleka kwa ogwira ntchito pofuna kuti athandizidwe mofulumira komaso mosatsata malamulo.

“Ndife osinthika musadzabwerenso ndi ziphuphu kuno!!!” awa ena mwa mawu omwe alembedwa pa chikwangwanichi cha DRTSS.

Pa chithuzi cha chikwangwani chomwecho, nthambi ya DRTSS yalimbikitsa anthu kuti azikanena ku bungwe lothana ndi ziphuphu la Anti Corruption Bureau (ACB) pomwe awona kapena kuganizira kuti ku ma ofesi awo kukuchitika ziphuphu.

“Mchitidwe uliwonse woganiziridwa kuti ndiwakatangale uyenera kukaneneledwa kwa akuluakulu aku DRTSS kudzera pa nambala yaulele ya 4040 komaso ku bungwe la Anti Coruption Bureau pa nambala ya ulele ya 113,” yatelo mbali ina yauthenga pa chikwangwani cha DRTSS omwe tautanthauzira m’chichewa.

Chikwanganicho chatsindika kuti chitetezo cha pamsewu ndi chinthu choyambilira chomwe nthambiyo imayika patsogolo kwambiri.

Pakadali pano anthu akupeleka maganizo osiyanasiyana pa uthengawu ndipo ena ati iyi ndi njira yabwino yowonetsa kusintha koma ena akuti kusintha kukuyenera kuyambira mumtima.

“Zimatengera kulimba mtima kwakukulu kuvomereza, kusintha ndi kuitana kuyang’anira. Ndikukhulupirira kuti uku ndikusintha kuchokera mu mtima, kusintha kwa zikhalidwe sikungosintha malo olakwira. Ndiye tithandizeni Mulungu!!” Watelo munthu wina pa thwita muuthenga omwe unalembadwa mchizungu.

DRTSS ndiimodzi mwa nthambi za boma zomwe m’mbuyomu zakhala zikutchuka kwambiri ndi nkhani za ziphuphu komaso katangale.

Nthambi ya DRTSS inakhazikitsidwa kuti iziwongolera kayendedwe kabwino ka pansewu powonetsetsa kuti malamulo apansewu akutsatidwa komaso kupereka maphunziro a za pansewu kwa nzika.

Follow us on Twitter:

Advertisement