Ana asanu ndi m’modzi osakwana zaka 14 ku Thyolo akulelana okhaokha

Advertisement

Pomwe mabanja ena akusowa ana palinso mabanja ena akuthawa udindo wao wopereka chisamaliro kwa ana awo obereka okha mdziko muno.

Ana awiri, Loveness ndi Liviness Weremu omwe ndi amapasa azaka 13, m’mudzi mwa Jolichi mfumu yaikulu Mchilamwera ku Thyolo akulera abale awo anayi popeza makolo awo adawathawa.

Loveness ndi Liviness adasiya sukulu mu sitandade 3 ndipo pano amagwira maganyu kuti apeze chokudya chothandidzira azing’ono awo ndi alongo awo omwe ndi achichepere.

Iwo adawuza Malawi24 kuti akukumana ndi mavuto oposa msinkhu wawo ndipo nthawi zina ngati asapeze maganyu amagona ndi njala chifukwa chosowa chokudya.

Iwe adati makolo awo adawathawa kalekale popeza amangokhalira kumwa mowa ndipo adangochoka pakhomopo. Mphekesera zikumveka kuti makolowa akungoyendayenda pa town ya Thyolo Boma lomwelo

Anawa omwe akuwoneka kuti akuvutika kuti apedze chokudya komanso zovala, nyumba yabwino yogona komanso kupita ku sukuulu akupempha anthu akufuna wabwino kuti awathandidze pamavuto omwe akukumana nawo.

Mpingo wa Everlasting Life Ministry Church ndiwomwe udawapedza anawa mdera la Khonjeni kwa T/A Chilamwera pomwe adapita mdelaro kukalalikira mau a Maulungu.

M’modzi mwa khristu wa Mpingo wa Everlasting Life Ministry Mai Mukile Rachel Mhango adafotokozera Malawi24 kuti mpingo wao ndiwokhudzidwa kwambiri powona momwe anawo akumvutikira.

Mai Mukile Mhango adapempha mabungwe komanso anthu akufuna kwabwino kuti alowelerepo pothandiza anawa ndipo akadakondwa  makolowo akadagwidwa ndikuzengedwa mlandu.

Follow us on Twitter:

Advertisement