Ng’ombeyagwada ndi mkulu watsopano wa ndende

Advertisement

Nthambi ya Malawi Prisons Service ili ndi mkulu watsopano ndipo mkuluyu ndi komishonala Masauko Ng’ombeyagwada Wiskot yemwe walowa pa udindowu kuyambira pa 25th March 2023.

Ofalitsa nkhani za Malawi Prisons Service mchigawo cha kummawa Sub Inspector Jones Nyasulu watsimikiza zakusankhidwa kwa komishonala General Masauko Ng’ombeyagwada Wiskot.

Komishonala Wiskot alowa mmalo mwa komishonala Grace Wandika Phiri omwe awasankha kukakhala mlembi wamkulu mu ofesi ya pulezidenti ndi Nduna.

Asadawasankhe paudindowu, a Ng’ombeyagwada adali kugwira ntchito ngati mkulu woyendetsa zinthu kunthambiyi.

Malingana ndikusintha kwa ntchito zanthambi za Malawi Prisons Service mkulu wanthambiyi tsopano adzitchedwa Commissioner General osatinso Chief Commissioner monga momwe zidalili poyamba.

Follow us on Twitter:

Advertisement