Akhristu ku Zomba achita Njira ya mtanda mogwirizana

Advertisement

Akhristu a mpingo wa Katolika ku St Charles Lwanga Parish mu Diocese ya Zomba mogwirizana ndi akhristu aku St George’s Anglican Parish mu Diocese ya Upper Shire lero adachita mapemphero a njira ya mtanda mu mzinda wa Zomba pokumbikira kufa kwa Ambuye Yesu pamtanda

Motsogodzedwa ndi a Vicar General a Diocese ya Zomba Fr. Vincent Chilolo komanso Archdeacon Fr. Christopher Mizaya ampingo wa Anglican, mapempherowa adayambira ku St Charles Lwanga Parish ndipo adayenda mpaka kukafika ku St George’s Anglican Parish.

Poyankhula pamwambowo, Fr Chilolo adapempha akhristu kuti adziwonetsa chikondi kwa anzawo potengera chikondi chomwe Mulungu adachiwonetsa pakati pathu potumiza mwana wake kudzatifera ife pamtanda.

Pamenepa Fr. Chilolo adapempha akhristu kuti adzithandidzana wina ndi nzake ndipo achotse chidani chilichonse mumtima mwao. Iwo adapemphanso akhristu kuti apewe kuchita zakatangale kumalo awo ogwilira ntchito popeza katangale ndiyemwe akuwononga mdziko lino.

Fr. Chilolo adayamikiranso mgwirizano omwe ulipo pakati pa mpingo wakatolika wa St Charles Lwanga Parish komanso mpingo wa Anglican wa St George’s Anglican Parish wopangira njira yamtanda limodzi chaka chilichonse ndipo adapempha kuti zimenezi zipitilire popedza ndizomwe Mulungu amafuna.

Mu mau ake, Archdeacon Fr Christopher Mizaya ampingo wa Anglican adati Ambuye Yesu adapereka nsembe pakati pathu choncho imfa yake itiphunzitse chikondi pakati pathu ndipo tikhale ndi mtima oganidzira ena pomwe ali pamavuto.

Fr Mizaya adapemphanso kuti akhristu apewe kuwononga zachilengedwe popeza kuwononga zachilengedwe kumabweretsa mavuto pakati pathu.

Follow us on Twitter:

Advertisement