Chilima sanaletsedwe kuyendera anthu – Kunkuyu

Advertisement
Malawi Vice President

A boma atsutsa mphekesera zomwe zikumveka zoti wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima analetsedwa kutulukira a Malawi amene akhudzidwa ndi mphepo ya namondwe ya Freddy.

A Malawi ambiri akhala akudabwa kuti mtsogoleri wa chipani cha UTM amenenso ali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko a Saulos Chilima ndi wa ndale ekhayo amene wabindikira.

Pa masamba a mchezo, nkhani yabuka ndi yoti a boma analetsa a Chilima kuzonda a Malawi ati poopa kuti angawalande shaini a Chakwera. Izi zinali makamaka pa chifukwa choti mmene ngoziyi imagwa, a Chakwera anali ali koyenda ku mayiko ena.

Koma polankhulapo pa nkhaniyi, mneneri wa boma a Moses Kunkuyu ati a Chakwera kapena a boma sanaletse a Chilima kuyendera anthu.

“Iyi ikutchedwa operation Tigwirane manja, sitikuyang’ana kuti akuthandiza anthu ndi ndani. Kaya ndi a Malawi, kaya ndi a kunja, aliyense akupemphedwa kuthandiza anthu,” anatero a Kunkuyu pouza wailesi ya Times.

Iwo anaonjezerapo kuti ngakhale atsogoleri otsutsa boma anthu akhala akuwaona akutulukira anthu ndi kuwathandiza.

“Kukanakhala koletsa anthu si mwina akanaletsedwa ndi amenewo?” anatero a Kunkuyu. “Koma a Chakwera anena kuti pano tonse tigwirane manja.”

Atapanikizidwa ndi mtolankhani Brian Banda kuti ndi chifukwa chani a Chilima sakuoneka pamene ena onse akuoneka, a Kunkuyu adanena kuti iwo sangathe kudziwa koma anakanitsitsa zoti a Chilima aletsedwa

Advertisement