Chakudya chavuta mu ndende za mdziko lino

Advertisement

Chakudya chavuta mu ndende za mdziko lino pomwe akaidi akungodya nyemba zokha kapena phala chifukwa cha kukwera kwa mitengo kwa zinthu m’dziko.

Ndizachidziwikire kuti kudya kwa kundende kumakhala kosiyaniranatu ndi mmene anthu ena omwe sali mndende amadyera, koma vutoli lafika pamwana wakana phala pomwe pano akaidi akumangodya nyemba zophika komanso phala.

Izi zadza kamba kakuti operekera zakudya ku ndende zosiyanasiyana mdziko lino akhala akudandaula kuti mitengo yazinthu yakwera ndipo akufuna kuti akweze mitengo yomwe amagulitsira malonda awo monga chimanga, nyemba ndi zakudya zina mndendezi, ndipo izi malingana mneneri wa ndende za mdziko lino a Chimwemwe Shaba zinakakamiza mthambi yowona ntchito za ndende kuti isake operekera zakudya ena chifukwa omwe amaperekera kalewa akumaperekera zakudya zochepa enanso anasiya kumene kuperekeraku.

“Ndi zoonadi kuti tili ndivuto lazakudya mndende zanthu zambiri, nkhani ndiyonena kuti azanthu omwe amatipatsa zakudya amene timati ma sapulayazi, akhala akudandaula kunena kutino mitengo yazinthu yakwera ndipo amafuna kuti tiakwezere mitengo, tinayesa kukamba nawo kuti malingana ndi ma mbajeti athu nzovutirapo nde takhala tikusaka ma sapulaya ena, koma kanyengo kameneka kosaka enaka zapezeka kuti ena mwaoperekera zakudya amaperekera chakudya chochepa mundende zanthu enanso anasiyiratu,” iwo anatero.

Koma a Shaba anonjezera kunena kuti mothandizana ndi anthu owona ntchito zachipatala akaidi omwe ali pa ndondomeko yomwa mankhwala a matenda a HIV ndi AIDS komanso Chifuwa chachikulu (TB) akusamalidwa bwino pa nyengo yakusowa chakudya mu ndendeyi.

Kumpoto kwa dziko lino kuli ndende m’maboma monga Karonga, Mzuzu, Nkhata Bay, Rumphi komanso Mzimba.

Ku chigawao chapakati ndende zili ku Kasungu, Ntcheu, Lilongwe, Dedza ndi Nkhotakota pamene kum’mawa kuli Mangochi, Domasi, Zomba Central Prison, Mikuyu ndi Mpyupyu ndipo kumwera kuli Mwanza, Luwani, Chikhwawa, Mulanje, Thyolo, Bvumbwe, Blantyre, Bangula, Nsanje ndi Makande.

Ndende zonsenzi padakali pano zikusungira chiwerengero cha akaidi osachepera 13,000.

Chiyambileni chaka chino mitengo ya zinthu yakwera kwambiri ndipo kukweraku kunaonjezereka mu June pomwe boma linatsitsa mphamvu ya ndalama ya Kwacha.

Follow us on Twitter:

Advertisement