Owina Lotto agula nyumba ndi galimoto

Advertisement

By Gracious Zinazi

Mdala Mkwinda wa zaka 57 yemwe anapata 45 million kwacha chifukwa analosera molondola ma nambala folo mu Premier Lotto wagwiritsa ntchito zina mwa ndalamazi pogula nyumba ndi galimoto.

Iwo agula nyumba yapamwamba ya 30 million kwacha ku Kanjedza mu mzinda wa Blantyre ndi galimoto yandalama zokwana 5 million kwacha.

Mzibamboyu yemwe ndi oyendetsa galimoto ku Blantyre City Council  anakhala munthu oyamba m’Malawi muno kupambana mphoto yaikulu chotero kuchoka ku Premier Lotto.

Koma ngakhale anawina, mkuluyu yemwe ndi okwatira komanso ali ndi ana anayi walangiza anthu kuti akhale olimbikira ntchito osati azigodalira mayere kapena kuti kubeta.

“Ndinapambana ndalama zankhaninkhani ngakhale sindichita mayere a Premier Bet pafupipafupi, ndimachita izi nthawi yanga yopuma pamene ndamaliza zomwe zimandipindulira m’moyo uno. Tiyeni tizi beta koma mosamalitsa,” anatero Mkwinda.

Advertisement