Wolemba: Gracious Zinazi
Lilongwe District Council kudzera mwa bwanankubwa wake Dr Lawford Palani, yaitanitsa msonkhano okhudza nkhani ya ulaliki wa m’busa Hamilton Yasin Gama yemwe wakwiyitsa anthu a mtundu wa Chewa chifukwa chowanyazitsira chikhalidwe chawo.
Ku msonkhanowu aitanitsa Kalembera wankulu wa C.C.A.P Nkhoma Synod, a Chewa Heritage, Chairperson wa Chiefs Forum mu boma la Lilongwe, Traditional Authority Chitukula ndi mafumu ena, komanso akuluakulu aku Lilongwe Police ndipo ukuyembekezereka kukhalapo lero pa February 24, 2022 nthawi ya 2 koloko masana ku Lilongwe District Council Chamber.
Msonkhanowu ukudzanso pomwe yemwe amalumikizanitsa mtundu wa achewa pakati pamaiko a Malawi, Mozambique komanso Zambia, Senior Chief Lukwa wati; a Reverend H. Yassin Gama apepese chifukwa chamawu omwe iwo anayankhula mukanema wina yemwe anthu akugawana pamasamba anchezo, chifukwa iwo anyonzetsa chikhalidwe cha achewa.
Masiku apitawa anthu pa masamba amchezo maka a Whatsapp akhala akugawana kanena wina yemwe akuonetsa Reverend Gama akufotokonza kuti anthu tikuyenera kukhala okhululuka.
“…tizichita ngati atate wanthu wakumwamba, amagwetsera mvula pa anthu oipa, midzi yanyawu pano ikulandira mvula, kudambwe kumene amavalira akakhwikhwi kumeneko mvula ikugwa mpaka zilembwe zanyowa kumeneko…” anatero a Gama mukanemayo.
Chewa Heritage Foundation yati ikomana ndi Reverend Gama kuti akambirane za nkhaniyi yomwe mamembala ena agule wamkulu sinawasangalatse.
Moderator wa Nkhoma CCAP Synod, Reverend Philip Kambulire wavomereza kuti wamuonadi kanemayu, koma akuyenera kufufuza zankumano omwe ukuyembekezeka kukhalapo pakati pa a Gama ndi a Chewa Heritage Foundation.
Reverend Yassin Gama amatumikira pa tchalitchi ya Mvama CCAP ku Lilongwe, ndipo mukanthawi kochepa adziwika chifukwa cha makanena ammasamba achenzo momwe iwo akumaoneka akulalikira mauthenga osiyanasiyana; olangiza mabanja, achinyamata, ndi ena.