Joshua Mbele waitanitsa zionetsero zoikira kumbuyo Martha Chizuma

Advertisement

M’modzi mwa anthu oyankhulapo pazinthu zosiyanasiyana makamaka pa masamba a mchezo a Joshua Chisa Mbele, ayitanitsa zionetsero sabata yamawa powonetsa kusakondwa ndi zomwe mkulu wa bungwe la Anti-Corruption Bureau, Martha Chizuma akukumana nazo.

Kuitanitsidwa kwa zionetselozi kukutsatira zomwe wachita yemwe akuganizilidwa kuti wakhala akuchita katangale a Ashok Nair omwe akasumira a Chizuma pankhani ya zomwe ankakambirana ndi munthu wina pafoni.

A Nair ati akasumira a Chizuma kaamba kowaipitsira mbiri pakuwatchula mu zokambirana zawozo kuti iwo anachita katangale kuti amasulidwe pomwe anamangidwa pankhani yokhudza katangale.

Koma izi zakwiyitsa a Malawi ambiri kuphatikizapo a Joshua Chisa Mbele omwe ayitanitsa zionetsero zomwe zikachitikile mumzinda wa Lilongwe sabata ya mawa lachitatu pa 2 March, 2022.

A Mbele pomwe amalengeza za zionetserozi patsamba lawo la facebook, ati akhazikitsa gulu lomwe akulitchula kuti ‘Citizens Against Impunity & Corruption’ lomwe ati cholinga chake ndikukakamiza adindo kuti achitepo kanthu pankhani yothana ndi katangale.

Mkuluyu watiso ndizodandaulitsa kuti munthu amene akuganizilidwa kuti wakhala akuchita za katangale akasumile omumanga ndipo ati izi ndichisonyezo choti a Nair akudelera kuti sangalandire chilango pamlandu omwe akuganiziridwa.

“Boma ili silili siliyasi pankhani zofuna kuthana ndi katangale ndipo zizindikiro zonse zaoneka tsopano. Ino ndi nthawi yoti tibwezeretse mzimu wa dziko lathu lokongola kwa a Malawi eni ake, dziko lino ndi la anthu. Ndiye zionetsero zilipo sabata yamawa lachitatu pa 2 March ku Lilongwe.

“Ino ndi nthawi yoti tiyankhule liwu limodzi potsutsana ndi mtudzu komaso katangale. Zomwe zikuchitika pa Martha Chizuma ndizoti anthu achita kugwirizana ndi cholinga choti ntchito yake ithe,” watero Mbele.

A Mbele anawonjezera kuti akhala akuyankhula kwa nthawi yaitali pankhani zofuna kuthana ndi katangale makamaka pakati pa akuluakulu a boma ndipo ati ino ndi nthawi yoti achitepo kanthu tsopano.

Mkuluyu yemwe amadziwikaso ndi dzina loti mneneri Yoswa, watsindika zakufunika koti a Malawi akhale ogwilizana komaso akhale mbali ya Chizuma ndi cholinga choti onse omwe akhala akuba ndalama za boma alandile chilango.

Iwo atiso sabata ino isanathe awonetsetsa kuti akhale atapeleka makalata ku khonsolo ya mzinda wa Lilongwe yowadziwitsa za zionetserozi zomwe zikuoneka kuti anthu ali nazo chidwi potengera ndi m’mene ambiri akuyankhulira pa masamba amchezo.

Pakadali pano bungwe lomenyera ufulu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lati nalo layima njii pambuyo pa a Chizuma ponena mayiyu ali ndikuthekera kothetsa katangale mdziko muno.

Advertisement