Galimoto za Porsche, Lamborghini zaonongeka ndi moto mu sitima yapamadzi


Wolemba: Gracious Zinazi

Galimoto pafupifupi 4,000 za mtundu wa Porsche, Volkswagen, Lamborghini ndi zina zaonongeka ndi moto omwe wayaka mu sitima ina ya pamadzi pa nyanja yaikulu ya Atlantic.

Sitimayi yomwe dzina lake ndi Felicity Ace, imachokera ku Emden mu dziko la Germany ndipo yayaka moto pafupi ndi zilumba za Azores mu dziko la Portugal.

Nyuzipepala ina yaku Germany yotchedwa Handelsblatt yati sitimayi inanyamula magalimoto okwana 3,965 omwe mwa ena ndi monga Audi, Lamborghini ndi ma Bentley.

Oyendetsa komanso othandizira mu sitimayi apulumutsidwa onse. Asilikali aku Portugal ati palibe wavulala pamene motowu unayaka  lachitatu lapitali.  Ogwira ntchito  mu sitimayi onse 22 apulumutsidwa ndipo ali ku hotel ina mu dzikolo.

“Mwini wa sitimayi Felicity Ace, akulumikizana ndiyemwe amayendetsa zaulendowu ndi cholinga choti akaichotse sitimayi pomwe ilipo” Anatero asilikali aku Portugal.

Malingana ndi nyupepala ya Handelsblatt, uthenga wapa e-mail kuchoka ku kampani yopanga galimoto yaku United States of America (U.S.A) Volkswagen wati  sitimayi inanyamula galimoto 3,965 zomwe ndi VW, Porsche, Audis komanso Lamborghini.  Volkswagen sinatsimikize kuti galimoto zake zinalimo zingati koma Porsche yati ake analimo 1,100 ndipo Bentley yati ake analimo 189.

“Tikulumikizana ndi kampani ya sitimayi kuti timve zambiri pa nkhaniyi”  anatero olankhulira kampani ya Volkswagen.

Malingana ndi website ya Marine traffic, sitima ya Felicity Ace imapita ku mafakitale a Volkswagen omwe ali ku  Davisville ku Chilumba cha Rhode.