Aphungu apempha kugulilidwa ma khotholo


A Malondera

Aphungu a nyumba ya malamulo mdziko muno apempha boma kuti lilingalire zowagulira ma khotholo kuti asamanyowe pomwe akukalowa mnyumbayi kuchokera pa malo osungira ma galimoto.

Izi ndimalingana ndi phungu wadera lakummwera chakummawa kwa boma la Lilongwe a Steven Malondera omwe anapititsa nkhaniyi ku nyumba ya malamulo pazokambirana za lachitatu pa 16 February, 2022.

Malingana ndi a Malondera, zovala zoteteza kuti usanyowezi ndizofunika kwambiri kwa aphunguwa makamaka nyengo ya mvula ngati ino.

Iwo anauza nyumba ya malamuloyi kuti aphunguwa azivala ndikugwilitsa ntchito ma khotholowa pomwe atsika galimoto zawo pa malo osungira magalimoto ku nyumba ya malamuloyi kukalowa m nyumba ya malamulo.

Ndipo poyankhulapo pa pempho la a Mulondera, mtsogoleri wa nyumbayi a Richard Chimwendo Banda, anayamikira phungu nzawoyu ponena kuti ganizo lawoli ndilofunika kwambiri.

A Chimwendo Banda ati iwo akayisiya nkhaniyi ku komishoni ya nyumbayi komwe akuluakulu ake akuyenera kukazukuta ganizoli ndikupeleka maganizo awo.

Koma pakadali pano a Malawi ambiri makamaka pamasamba amchezo, adzudzula phunguyu kaamba kaganizoli ndipo ambiri akuti izi sizikuyenera kuchitika.

Anthu ambiri akuti ndi bwino kuti ndalama zogulira ma khotholowa zigwire ntchito yothandizira anthu omwe akhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi mmadera ambiri mdziko muno kaamba ka namondwe wa Ana.

A Herbert Chawinga ndi mmodzi mwa anthu omwe akutsutsana ndi ganizoli ndipo anena kuti; “koma zoona phungu yemwe amalandira kale ndalama zambiri azikapempha kugululidwa ma khotholo mmalo mopempha malata okafolelera nyumba za anthu omwe akhudzidwa ndi madzi osefukura?

“Aphunguwa apambana chiyani kuti mpaka agulilidwe izi mmalo moonetsa utsogolera odzipeleka pothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi madzi osefukira? Izi ndizodandaulitsa kwambiri.”

Anthu enaso adzudzula aphunguwa pobweretsa ganizoli pomwe chuma chadziko lino sichikuyenda bwino ndipo ati ngatidi boma limanva zoyankhula za mzika zake, silikuyenera kuvomera pempholi.